SHARE


Pamene zokambilana za aphungu ku nyumba ya malamulo zangoyambapo, mtsogoleri wa zipani zotsutsa a Lazarus Chakwera anena kuti iwo ndi anzawo ayambapo kunyanyala zokambilanazo.

Malinga ndi a Chakwera amenenso ali mtsogoleri wa chipani chotsutsa cha Kongeresi, iwo ndi aphungu awo ati ayamba kunyanyala zokambilanazo ngati a boma sabweletsa mu nyumbayo nkhani yokhudza zisankho.

Lazarus Chakwera

Chakwera: A Mutharika ndi a bodza.

A Chakwera adaulula izi pamene amayankhapo pa zimene a Mutharika adakamba potsegulila nyumba ya malamulo lachisanu.

“Ndipo a Mutharika ndi abodza, anatilonjeza kuti abweletsa nkhani yokhudza malamuo a zisankho, koma mmalo mwake tikuona palibepo,” anatelo a Chakwera.

“Ndipo ife tikunena lero kuti ngati nkhani imeneyi siyibwela pano, ife tiyamba kunyanyala zokambilana mu nyumba ino,” a Chakwera anaopseza motelo.

Mwa zina, malamulo a tsopano ovotela akunena kuti munthu opambana chisankho cha President azikhala kuti wapeza mavoti opyolera theka la mavotiwo.

Zikuoneka ngati chipani cholamula cha DPP ndi a Mutharika sakukondwa nazo zina mwa nkhanizi.

 

 

 

 Source link

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here