Zambiri zakhala zikukambidwa za mkalabongo, mowa waukali umene suchedwa kutenga amene akuumwa koma tsopano, makampani 21 akufufuzidwa pamadandaulo amene Amalawi amakhala nawo.

M’sabatayi, bungwe loona za chilungamo pa malonda la Competition and Fair Trade Commission (CFTC) lidatulutsa chikalata chopempha Amalawi kupereka madandaulo awo pa makampani otcheza mkalabongowo.

Akuluaku a mabungwe amene akhala akulimbana ndi mowawo, umene poyamba unkatchedwa kuti masacheti, akondwa chifukwa CFTC ikufufuza makampaniwo. CFTC idakhazikitsidwa ndi malamulo oteteza ogula m’dziko lino.

Mkulu wa bungwe la Young Achievers for Development (YAD) Jefferson Milanzi adati nkhaniyi tsopano ikusongola ndipo izi zimayenera kuchitika padzana.

“Dziko la Malawi ndi laling’ono kwambiri choncho n’zodabwitsa kuti tili ndi makampani 21 otcheza mowa umene waika miyoyo pachiswe, kusokoneza chitukuko komanso maphunziro. Iyi ndi nkhani yabwino,” adatero Milanzi.

Iye adati kuchuluka kwa makampaniwo kukungosonyeza kuti amaika mtima pa ndalama zomwe amapeza, osati miyoyo ya Amalawi.

Mkulu wa bungwe lothana ndi mankhwala wozunguza ubongo la Drug Fight Malawi, Nelson Zakeyu, wati mkalabongo ndi mowa womwe umafulidwa mosatsata ndondomeko popeza ukali wake umafika 47 peresenti, omwe ndi wosavomerezeka ndi bungwe loona zaumoyo wa anthu padziko lonse la World Health Organisation (WHO).

“Izi zikusemphananso ndi mfundo yachitatu ya chitukuko ya bungwe la United Nations makamaka gawo 3 ndime 3.5 yomwe imalimbikitsa umoyo wabwino pothana ndi uchidakwa, kusuta fodya ndi zina.

 “Akatswiri a zaumoyo a WHO omwe tikugwira nawo ntchito adatiuza kuti mowawu umaononga ubongo, mapapo, impso, komanso kulumalitsa nkhope,” adatero Zakeyu.

Mkuluyu adati mkalabongo waika pachiopsezo miyoyo ya ana ndi achinyamata ambiri popeza umagulitsidwa mtengo wotsika woti aliyense atha kuufikira.

Zakeyu adati kafukufuku wa CFTC ateteza anthu ku mavuto omwe amadza akamwa mkalabongo.

“Kampani zambiri zimabisa ukali weniweni wa mowawu. Zotsatira za kafukufuku wa ophunzira a m’sukulu zaukachenjede za ku Norway ndi Chancellor College mu 2010 adaonetsa kuti achinyamata akusokonekera chifukwa cha mkalabongo.

“Malingana ndi kafukufukuyo, izi zikulimbikitsa umphawi m’dziko muno chifukwa anthu omwe amamwa mowamu sakhala nzika zopanga ziganizo zothandiza potukula dziko,” adatero Zakeyu.

M’chikalata chomwe CFTC yatulutsa ndipo chasayinidwa ndi mkulu 

wa bungweli, Wezi Malonda, chikuti CFTC yalandira madandaulo oti mowawu ulibe zizindikiro zovomerezeka ndi Malawi Bureau of Standards (MBS).

Izi zili choncho, zidakwa zina za ku Ndirande mumzinda wa Blantyre zauza Msangulutso kuti mowawu wasokoneza kwambiri miyoyo yawo.

Bright Katuli, mmodzi mwa anyamata a pamsika wa Ndirande, adati amakonda kachasu poyerekeza ndi mkalabongo.

“Timamwa mkalabongo chifukwa chotsika mtengo, koma siwabwino. Mowa wina uliwonse umafuna kudyera, koma mkalabongo umachotsa chilakolako cha chakudya. Ichi n’chifukwa chake ena amafa nawo.

“Munthu ukamwa mkalabongo amadzuka thupi likuphwanya, komanso ali ndi ludzu lofuna kumwa wina,” adatero Katuli.

Ndemwene Kazonde ndi Moses Kachisa akugwirizana ndi Katuli ndipo apempha boma kuti liletse mowawu popeza ukuononga anthu.

“Sungapeze zigubu za mkalabongo pamalo omwera mowa kaamba koti umagulitsidwa mwachinyengo. Tikungomwera ugonthi, kuipa kwake tikukuona.

“Mkalabongo ndi wautsiru moti panopa maso anga satha kuona bwino patali. Anzathu ena zochita n’zobalalika pamene ena akulumala nkhope chifukwa cha mowawu,” adateto Kachisa.

M’chikalatacho, Malonda adati: “Sitikunena kuti kampani zomwe tikufufuzazi zaphwanya malamulo. Tikufuna kupeza ngati madandaulo omwe talandira ali woona, komanso ngati kampanizo zikuphwanya malamulo. Tikufuna kupeza ngati mowawu ukuonononga miyoyo ya anthu, komanso tikufuna kudziwa ngati kampanizo zikutsatira ndondomeko zonse zotetezera miyoyo ya anthu.

“Kupezeka kwa chizindikiro cha MBS pamowa kumatsimikizo kuti mowawo wakwanitsa malamulo onse omwe boma lidaika pofuna kuteteza miyoyo ya anthu,” yatero kalatayo.

Koma titayesa kuimba manambala atatu amene adaikidwa pa mabotolo a mkalalabongo osiyanasiyana kuti timve mbali ya makampaniwo, palibe yomwe imagwira. n

Source link

LEAVE A REPLY